Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Malaki 2:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu.

2. Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale cifukwa simuliika mumtima.

3. Taonani, ndidzaipsa mbeu cifukwa ca inu, ndi kuwaza ciphwidza pankhope panu, ndico ciphwidza ca nsembe zanu, ndipo adzakucotsani pamodzi naco.

4. Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti cipangano canga cikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.

5. Cipangano canga cinali naye ca moyo ndi ca mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa cifukwa ca dzina langa.

6. Cilamulo ca zoona cinali m'kamwa mwace, ndi cosalungama sicinapezeka m'milomo mwace; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu,

7. Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga cidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna cilamulo pakamwa pace; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Malaki 2