Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Malaki 1:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe coipa! ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe coipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? kapena adzakubvomerezani kodi? ati Yehova wa makamu.

9. Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti aticitire cifundo; icico cicokera kwa inu; kodi Iye adzabvomereza ena a inu? ati Yehova wa makamu.

10. Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto cabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira capereka m'dzanja lanu.

11. Pakuti kuyambira koturukira dzuwa kufikira kolowera kwace dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa cofukiza ndi copereka coona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

12. Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zace, cakudya cace, conyozeka.

13. Mukutinso, Taonani, ncolemetsa ici! ndipo mwacipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu? ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Malaki 1