Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 9:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, tsiku lacisanu ndi citatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ace amuna, ndi akuru a Israyeli;

2. ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwana wa ng'ombe wamwamuna, akhale nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda cirema, nubwere nazo pamaso pa Yehova.

3. Nunene kwa ana a Israyeli, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yaucimo; ndi mwana wa ng'ombe, ndi mwana wa nkhosa, a caka cimodzi, opanda cirema, akhale nsembe yopsereza;

4. ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosanganiza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.

5. Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa cihema cokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova,

6. Ndipo Mose anati, Ici ndi cimene Yehova anakuuzani kuti mucicite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 9