Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 7:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zace tsiku lacitatu, sikubvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo cinthu conyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zace.

19. Ndipo nyama yokhudza kanthu kali konse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama yina, ali yense ayera aidyeko.

20. Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala naco comdetsa, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

21. Ndipo munthu akakhudza cinthu codetsa, codetsa ca munthu, kapena codetsa ca zoweta, kapena ciri conse conyansa codetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

22. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

23. Lankhula ndi ana a Israyeli ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng'ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi.

24. Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi cirombo ayenera nchito iri yonse, koma musamadya awa konse konse.

25. Pakuti ali yense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

26. Ndipo musamadya mwazi uti wonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse,

27. Ali yense akadya mwazi uti wonse, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

28. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

29. Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yace kwa Yehova, azidza naco copereka cace kwa Yehova cocokera ku nsembe yoyamika yace;

30. adze nazo m'manja mwace nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 7