Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 6:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, ciwacokere ku nsembe zamoto za Yehova; ali yense wakuzikhudza izi adzakhala wapatolika.

19. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

20. Copereka ca Aroni ndi ana ace, cimene azibwera naco kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ici: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale copereka caufa kosalekeza, nusu lace m'mawa, nusu lace madzulo.

21. Cikonzeke paciwaya ndi mafuta; udze naco cokazinga; copereka caufa cazidutsu ubwere naco, cikhale pfungo lokoma la kwa Yehova.

22. Ndipo wansembe wodzozedwa m'malo mwace, wa mwa ana ace, acite ici; likhale lemba losatha; acitenthe konse kwa Yehova.

23. Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 6