Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 4:23-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace, ndico tonde wopanda cirema;

24. naike dzanja lace pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yaucimo.

25. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.

26. Ndipo atenthe mafuta ace onse pa guwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

27. Ndipo akacimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, naparamula;

28. akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace mbuzi yaikazi, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita.

29. Aike dzanja lace pamutu pa nsembe yaucimo, naiphe nsembe yaucimo pamalo pa nsembe yopsereza.

30. Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace wonse patsinde pa guwa la nsembe.

31. Nacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

32. Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo copereka cace, ikhale nsembe yaucimo, azidza nayo yaikazi, yopanda cirema.

33. Naike dzanja lace pa mutu wa nsembe yaucimo, ndi kuipha ikhale nsembe yaucimo pamalo pophera nsembe yopsereza.

34. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace wonse patsinde pa guwa la nsembe;

35. nawacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe, awa pa guwa la nsembe, monga umo amacitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amcitire comtetezera pa kucimwa kwace adakucimwira, ndipo adzakhululukidwa.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 4