Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 4:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. kukadziwika kucimwa adacimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng'ombe yamphongo, ikhale nsembe yaucimo, ndipo udze nayo ku khomo la cihema cokomanako.

15. Ndipo akuru a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

16. Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng'ombeyo ku cihema cokomanako;

17. nabviike cala cace m'mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, cakuno ca nsaru yocinga.

18. Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'cihema cokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.

19. Ndipo acotse mafuta ace onse, nawatenthe pa guwa la nsembe.

20. Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anacitira ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo wansembe awacitire cowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.

21. Ndipo aturutse ng'ombeyo kunja kwa cigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yaucimo ya kwa msonkhano.

22. Akacimwa mkuru, osati dala, pa cina ca zinthu ziti zonse aziletsa Yehova Mulungu wace, naparamula;

23. akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace, ndico tonde wopanda cirema;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 4