Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 4:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Naturutse cikopa ca ng'ombeyo, ndi nyama yace yonse, pamodzi ndi mutu wace, ndi miyendo yace, ndi matumbo ace, ndi cipwidza cace,

12. inde ng'ombe yonse, kunja kwa cigono, kumka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.

13. Ndipo khamu lonse la Israyeli likalakwa osati dala, ndipo cikabisika cinthuci pamaso pa msonkhano, litacita cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, ndi kuparamula;

14. kukadziwika kucimwa adacimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng'ombe yamphongo, ikhale nsembe yaucimo, ndipo udze nayo ku khomo la cihema cokomanako.

15. Ndipo akuru a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

16. Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng'ombeyo ku cihema cokomanako;

17. nabviike cala cace m'mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, cakuno ca nsaru yocinga.

18. Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'cihema cokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.

19. Ndipo acotse mafuta ace onse, nawatenthe pa guwa la nsembe.

20. Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anacitira ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo wansembe awacitire cowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.

21. Ndipo aturutse ng'ombeyo kunja kwa cigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yaucimo ya kwa msonkhano.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 4