Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 26:26-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Pamene ndityola mcirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mcembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.

27. Ndipo mukapanda kundimvera Ine, cingakhale ici, ndi kuyenda motsutsana nane;

28. Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.

29. Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya.

30. Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.

31. Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za pfungo lanu lokoma.

32. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.

33. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi midzi yanu idzakhala bwinja.

34. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ace, masiku onse a kupasuka kwace, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ace.

35. Masiku onse a kupasuka kwace lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo.

36. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapitikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.

37. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.

38. Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.

39. Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.

40. Pamenepo adzabvomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pocita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,

41. Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzicepetsa, ndipo abvomereza kulanga kwa mphulupulu zao;

42. pamenepo ndidzakumbukila pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isake, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukila; ndipo ndidzakumbukila dzikoli.

43. Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ace, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzabvomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 26