Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 26:23-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;

24. Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zoipa zanu.

25. Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakucita cilango ca cipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.

26. Pamene ndityola mcirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mcembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.

27. Ndipo mukapanda kundimvera Ine, cingakhale ici, ndi kuyenda motsutsana nane;

28. Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.

29. Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya.

30. Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.

31. Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za pfungo lanu lokoma.

32. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.

33. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi midzi yanu idzakhala bwinja.

34. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ace, masiku onse a kupasuka kwace, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ace.

35. Masiku onse a kupasuka kwace lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo.

36. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapitikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.

37. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 26