Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 25:32-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Kunena za midzi ya Alevi, nyumba za m'midzi yao yao, Alevi akhoza kuziombola nthawi zonse.

33. Ndipo munthu akagula kwa Mlevi, nyumba yogulayo yokhala m'mudzi wace wace, ituruke m'caka coliza lipenga, popeza nyumba za m'midzi ya Alevi ndizo zao zao mwa ana a Israyeli.

34. Koma dambo la podyera pao siligulika; popeza ndilo lao lao kosatha.

35. Ndipo mbale wako akasaukira cuma, ndi dzanja lace lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.

36. Usamambwezetsa phindu, kapena cioniezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.

37. Musamampatsa ndarama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pocibwezera.

38. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kukupatsani dziko la Kanani, kuti ndikhale Mulungu wanu.

39. Ndipo mbale wako akasaukira cuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa nchito monga kapolo;

40. azikhala nawe ngati wolipidwa nchito, ngati munthu wokhala nawe; akutumikire kufikira caka coliza lipenga.

41. Pamenepo azituruka kukucokera, iye ndi ana ace omwe, nabwerere ku mbumba yace; abwerere ku dziko lao lao la makolo ace.

42. Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.

43. Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.

44. Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo amuna ndi akazi.

45. Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anu anu.

46. Ndipo muwayese colowa ca ana anu akudza m'mbuyo, akhale ao ao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israyeli, musamalamulirana mozunza.

47. Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera cuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa pfuko la banja la mlendo;

48. atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ace amuombole;

49. kapena mbale wa atate wace, kapena mwana wa mbale wa atate wace amuombole, kapena mbale wace ali yense wa banja lace amuombole; kapena akalemera cuma yekha adziombole yekha.

50. Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira caka adadzigulitsa kwa iye kufikira caka coliza lipenga; ndipo mtengo wace ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 25