Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 25:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo mukadzati, Tidzadyanji caka cacisanu ndi ciwiri? taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;

21. pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu caka cacisanu ndi cimodzi, ndipo cidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.

22. Ndipo mubzale caka cacisanu ndi citatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira caka cacisanu ndi cinai, mpaka zitacha zipatso zace mudzadya zasundwe.

23. Ndipo asaligulitse dziko cigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.

24. Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo.

25. Mbale wako akasaukira cuma, nakagulitsa cace cace, pamenepo mombolo wace, mbale wace weni weni azidza, naombole cimene mbale wace anagulitsaco.

26. Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lace lacionetsa, nacipeza cofikira kuciombola;

27. pamenepo awerenge zaka za kugulitsa kwace, nabwezere wosulayo zotsalirapo, nabwerere iye ku dziko lace.

28. Koma dzanja lace likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo cogulitsaco cikhale m'dzanja lace la iye adacigulayo, kufikira caka coliza lipenga; koma caka coliza lipenga cituruke, nabwerere iye ku dziko lace.

29. Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m'mudzi wa m'linga, aiombole cisanathe caka coigulitsa; kufikira kutha caka akhoza kuombola.

30. Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwace kwa caka camphumphu, nyumba iri m'mudzi wa m'lingayi idzakhala yace ya iye adaigula yosamcokeranso mwa mibadwo yace; siidzaturuka caka coliza lipenga.

31. Koma nyumba za m'midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m'dziko; ziomboledwe, zituruke m'caka coliza lipenga.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 25