Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 24:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo anamsunga m'kaidi, kuti awafotokozere m'mene anenere Yehova.

13. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

14. Turuka naye wotembererayo kunja kwa cigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pace, ndi khamu lonse limponye miyala afe.

15. Ndipo unene ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Ali yense wotemberera Mulungu wace azisenza kucimwa kwace.

16. Ndi iye wakucitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akacitira dzina la Yehova mwano, awaphe.

17. Munthu akakantha munthu mnzace ali yense kuti afe, amuphe ndithu.

18. Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere yina; moyo kulipa moyo.

19. Munthu akacititsa mnansi wace cirema, monga umo anacitira momwemo amcitire iye;

20. kutyola kulipa kutyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anacitira munthu cirema, momwemo amcitire iye.

21. Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere yina; iye wakupha munthu, amuphe.

22. Ciweruzo canu cifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m'dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

23. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, ndipo anaturutsa wotembererayo kunja kwa cigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israyeli anacita monga Yehova adauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 24