Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 22:9-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Potero asunge cilangizo canga, angasenzepo ucimo, ndi kufera m'mwemo, pakuciipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo,

10. Mlendo asadyeko copatulikaco; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa nchito, asadyeko copatulikaco.

11. Koma wansembe atakagula munthu ndi ndarama zace, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yace, adyeko mkate wace.

12. Ndipo mwana wamkazi wa wansembe akakwatibwa ndi mlendo, asadyeko nsembe yokweza ya zinthu zopatulika.

13. Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wocotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera ku nyumba ya atate wace, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wace; koma mlendo asamadyako.

14. Ndipo munthu akadyako cinthu copatulika mosadziwa, azionjezapo limodzi la magawo asanu, nalipereke kwa wansembe, pamodzi ndi copatulikaco.

15. Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zopereka iwo kwa Yehova;

16. ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwaparamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.

17. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

18. Nena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana onse a Israyeli, nuti nao, Ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena wa alendo ali m'Israyeli, akabwera naco copereka cace, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;

19. kuti mulandiridwe, azibwera navo yaimuna yopanda cirema, ya ng'ombe, kapena nkhosa, kapena mbuzi.

20. Musamabwera nayo yokhala ndi cirema; popeza siidzalandirikira inu.

21. Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa cowinda cacikuru, kapena ya pa copereka caufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda cirema.

22. Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapenayodukamwendokapena yopunduka, kapena yapfundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukuru, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto pa guwa la nsembe.

23. Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yocepa ciwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa cowinda siidzalandirika.

24. Nyama yofula, kapena copwanya kapena cosansantha, kapena cotudzula, kapena codula, musamabwera nazo kwa Yehova; inde musamacicita ici m'dziko mwanu.

25. Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale cakudya ca Mulungu wanu; popeza ziri nako kubvunda kwao; ziri ndi cirema; sizidzalandirikira inu.

26. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi mace masiku asanu ndi awiri;

27. kuyambira tsiku lacisanu ndi citatu ndi m'tsogolo mwace, idzalandirika ngati copereka nsembe yamoto ya Yehova.

28. Koma musamaipha ng'ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wace tsiku limodzimodzi.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 22