Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 22:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Nena ndi Aroni ndi ana ace amuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.

3. Nena nao, Ali yense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azipatulira Yehova, pokhala ali naco comdetsa cace, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.

4. Munthu ali yense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo ali yense wokhudza cinthu codetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;

5. ndi ali yense wokhudza cinthu cokwawa cakudetsedwa naco, kapenanso munthu amene akamdetsa naco, codetsa cace ciri conse;

6. munthu wokhudza ciri conse cotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lace ndi madzi.

7. Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pace adyeko zoyerazo, popeza ndizo cakudya cace.

8. Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.

9. Potero asunge cilangizo canga, angasenzepo ucimo, ndi kufera m'mwemo, pakuciipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo,

10. Mlendo asadyeko copatulikaco; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa nchito, asadyeko copatulikaco.

11. Koma wansembe atakagula munthu ndi ndarama zace, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yace, adyeko mkate wace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 22