Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 21:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Asaipse mbeu yace mwa anthu a mtundu wace; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.

16. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

17. Nena ndi Aroni, kuti, Ali yense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala naco cirema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wace.

18. Pakuti munthu ali yense wokhala naco cirema, asayandikize; wakhungu, kapena wotsimphina, kapena wopunduka mph uno, kapena wamkuru ciwalo,

19. kapena munthu wopunduka phazi kapena wopunduka dzanja,

20. kapena wowerama, kapena wamfupi msinkhu, kapena wopunduka diso, kapena munthu wamphere, kapena wacipere, kapena wopunduka kumoto.

21. Wa mbeu ya Aroni wansembe asayandikize mmodzi wokhala naco cirema, kupereka nsembe zamoto za Yehova; ali naco cirema asayandikize kupereka cakudya ca Mulungu wace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 21