Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 20:18-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakambvula, anabvula kasupe wace, ndi iye mwini anabvula kasupe wa nthenda yace; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.

19. Usamabvula mbale wa mai wako, kapena mlongo wa atate wako; popeza anabvula abale ace; asenze mphulupulu yao.

20. Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa atate wace, nabvula mbale wa atate wace; asenze kucimwa kwao; adzafa osaona ana.

21. Munthu akatenga mkazi wa mbale wace, codetsa ici; wabvula mbale wace; adzakhala osaona ana.

22. Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwacita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo.

23. Musamatsata miyambo ya mtundu umene neliucotsa pamaso panu; popeza anacita izi zonse, nelinalema nao.

24. Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu yina ya anthu.

25. Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kali konse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.

26. Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.

27. Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamtu pao.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 20