Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu yina ya anthu.