Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 20:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Unenenso kwa ana a Israyeli ndi kuti, Ali yense wa ana a Israyeli, kapena wa alendo akukhala m'Israyeli, amene apereka mbeu zace kwa Moleke, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.

3. Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace; popeza anapereka a mbeu zace kwa Moleke, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.

4. Ndipo ngati anthu a m'dzikomo akambisa munthuyo pang'ono ponse, pamene apereka a mbeu zace kwa Moleke, kuti asamuphe;

5. pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lace, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi cigololo kukacita cigololo kwa Moleke, kuwacotsa pakati pa anthu a mtundu wao.

6. Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi cigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace.

7. Cifukwa cace dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

8. Ndipo musunge malemba anga ndi kuwacita; Ine ndine Yehova wakupatula inu.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 20