Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 2:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo munthu akabwera naco copereka ndico nsembe yaufa ya kwa Yehova, copereka cace cizikhala ca ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo libano.

2. Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi libano wace wonse; ndipo wansembeyo aitenthe cikumbutso cace pa guwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.

3. Ndipo cotsalira ca nsembe yaufa cikhale ca Aroni ndi ana ace; ndico copatulikitsa ca nsembe zamoto za Yehova.

4. Ndipo ukabwera naco copereka ndico nsembe yaufa, yophika mumcembo, cizikhala ca timitanda ta ufa wosalala topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda cotupitsa todzoza ndi mafuta.

5. Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m'ciwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda cotupitsa, wosanganiza ndi mafuta.

6. Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa.

7. Ndipo copereka cako cikakhala nsembe yaufa ya mumphika, cikhale ca ufa wosalala ndi mafuta.

8. Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera naco kwa wansembe, iyeyo apite naco ku guwa la nsembe.

9. Ndipo wansembeyo atengeko cikumbutso pa nsembe yaufa, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndico nsembe yamoto ya pfungo lokoma la kwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 2