7. Akakadya konse tsiku tacitatu kali conyansa, kosabvomerezeka:
8. koma ali yense akudyako adzasenza mphulupulu yace, popeza waipsa copatulidwa ca Yehova; ndi munthuyo amsadze, kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.
9. Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.
10. Usamakunkha khunkha la m'munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11. Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana.
12. Musamalumbira monama ndi kuchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
13. Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zace; mphotho yace ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.
14. Usamatemberera wogontha; usamaika cokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.