Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:15-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. ndipo wansembe atengeko muyeso wa mafuta, nawathire pa cikhato ca dzanja lace lamanzere la iye mwini;

16. ndipo wansembe abviike cala cace ca dzanja lace lamanja ca iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lace lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi cala cace pamaso pa Yehova;

17. ndipo wansembe apakeko mafuta okh a ria m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yoparamula;

18. natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lace la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amcitire comtetezers pamaso pa Yehova.

19. Ndipo wansembe apereke nsembe yaucimo, namcitire comtetezera amene akuti ayeretsedwe, cifukwa ca kudetsedwa kwace; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza;

20. ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa pa guwa la nsembe; ndipo wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhala iye woyera.

21. Ndipo akakhala waumphawi cosafikana cuma cace azitenga mwana wa nkhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yoparamula, aiweyule kumcitira comtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi wa mafuta;

22. ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yaucimo, ndi linzace la nsembe yopsereza.

23. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la cihema cokomanako, pamaso pa Yehova.

24. Ndipo wansembe atenge mwana wa nkhosa wa nsembe yoparamula, ndi muyeso wa mafuta, ndipo wansembe aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova;

25. naphe mwana wa nkhosa wa nsembe yoparamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yoparamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja;

26. ndipo wansembe athireko mafuta aja m'cikhato cace camanzere ca iye mwini;

27. ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lace lamanzere ndi cala cace ca dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova;

28. ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca: dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa usembe yoparamula;

29. ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumcitira comtetezera pamaso pa Yehova.

30. Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo, limodzi la nsembe yaucimo, ndi tina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa;

31. ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14