Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 13:51-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

51. naone nthenda tsiku lacisanu ndi ciwiri; ngati nthenda yakula pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pacikopa, ziri zonse zanchito zopangika ndi cikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndico codetsedwa.

52. Ndipo atenthe cobvalaco ngakhale muyaro wace, ngakhale mtsendero wace, caubweya kapena cathonje, kapena ciri conse cacikopa ciri ndi khate, ndilo khate lofetsa; acitenrhe ndi mote.

53. Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pacobvala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa;

54. pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke cija pali khate, nacibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena;

55. ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ace, yosakulanso nthenda, ndico codetsedwa; ucitenthe ndi moto; ndilo pfunka, kungakhale kuyera kwace kuli patsogolo kapena kumbuyo.

56. Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa cobvala, kapena cikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero;

57. ndipo ikaonekabe pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, irikubukanso; ucitenthe ndi moto cija canthenda.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 13