Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 10:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo anasendera pafupi, nawanyamula osawabvula maraya ao a m'kati, kumka nao kunja kwa cigono, monga Mose adauza.

6. Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi ltamara ana ace, Musawinda tsitsi, musang'amba zobvala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israyeli, alire cifukwa ca motowu Yehova anauyatsa.

7. Ndipo musaturuka pakhomo pa cihema cokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anacita monga mwa mau a Mose.

8. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, nati,

9. Usamamwa vinyo, kapena coledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'cihema cokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;

10. ndi kuti musiyanitse pakati pa copatulika ndi cosapatulika, ndi pakati pa codetsa ndi coyera;

11. ndi kuti muphunzitse ana a Israyeli malemba onse amene Yehova analankhula nao ndi dzanja la Mose.

12. Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ace otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda cotupitsa pafupi pa guwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulikitsa;

13. ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, locokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza cotero.

14. Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako amuna, zocokera ku nsembe zoyamika za ana a Israyeli.

15. Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nazo pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako amuna, mwa lemba losatha; monga Yehova anauza.

16. Ndipo Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yaucimo, ndipo, taonani, adaitentha.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 10