11. Kunena za Efraimu, ulemerero wao udzauluka ndi kucoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.
12. Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwacokera.
13. Efraimu, monga ndaona, akunga Turo, wookedwa pokoma; koma Efraimu adzaturutsira ana ace wakuwaphera.
14. Apatseni, Yehova; mudzapatsa ciani? muwapatse mimba yotayataya, ndi mawere ouma.
15. Coipa cao conse ciri m'Giligala; pakutipamenepo ndinawada, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe ao ndidzawainga kuwacotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.
16. Efraimu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao.
17. Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvera Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu.