7. Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kabvumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzaturutsa ufa; cinkana iuturutsa, alendo adzaumeza.
8. Israyeli wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati cotengera coti munthu sakondwera naco.
9. Pakuti anakwera kumka ku Asuri, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wace; Efraimu walembera omkonda ngati anchito.
10. Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kucepa cifukwa ca katundu wa mfumu ya akalonga.
11. Popeza Efraimu anacurukitsa maguwa a nsembe akucimwako, maguwa a nsembe omwewo anamcimwitsa.
12. Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za cilamulo canga, koma zinayesedwa ngati cinthu cacilendo.
13. Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukila mphulupulu yao, nadzalanga zocimwa zao; adzabwerera kumka ku Aigupto.
14. Pakuti Israyeli waiwala Mlengi wace, namanga akacisit ndipo Yuda wacurukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yace moto, nudzatha nyumba zace zazikuru.