Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 5:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Efraimu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wace kutsata lamulolo.

12. Ndipo ndikhala kwa Efraimu ngati njenjete, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati cibvundi.

13. Pamene Efraimu anaona nthenda yace, ndi Yuda bala lace, Efraimu anamuka kwa Asuri, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuciritsani, kapena kupoletsa bala lanu.

14. Pakuti ndidzakhala kwa Efraimu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kucoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.

15. Ndidzamuka ndi kubwerera kumka kumalo kwanga, mpaka adzabvomereza kuparamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwacangu.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 5