4. Koma munthu asatsutsane ndi mnzace, kapena kudzudzula mnzace; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe.
5. Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.
6. Anthu anga aonongeka cifukwa ca kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala cilamulo ca Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.
7. Monga anacuruka, momwemo anandicimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.
8. Adyerera cimo la anthu anga, nakhumbira cosalungama cao, yense ndi mtima wace.
9. Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga cifukwa canjira zao, ndi kuwabwezera macitidwe ao.
10. Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzacita cigololo, koma osacuruka; pakuti waleka kusamalira Yehova.
11. Cigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zicotsa mtima,
12. Anthu anga afunsira ku mtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wacigololo wawalakwitsa, ndipo acita cigololo kucokera Mulungu wao.