Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 3:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. M'mwemo ndinadzigulira iye ndi ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndi homeri ndi nusu wa barele;

3. ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usacita cigololo, usakhala mkazi wa mwamuna ali yense; momwemo inenso nawe.

4. Pakuti ana Israyeli adzakhala masiku ambiri a opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda coimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;

5. atatero ana a Israyeli adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wace masiku otsiriza.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 3