Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 10:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Adzacitengeranso ku Asuri cikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efraimu adzatenga manyazi, ndi Israyeli adzacita manyazi ndi uphungu wace.

7. Ndipo Samariya, mfumu yace yamwelera ngati thobvu pamadzi.

8. Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo cimo la Israyeli, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.

9. Israyeli, wacimwa kuyambira masiku a Gibeya; pomwepo anaimabe; nkhondo ya pa ana a cosalungama siinawapeza ku Gibeya.

10. Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri.

11. Ndipo Efraimu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lace lokoma; ndidzamsenzetsa Efraimu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya cibuluma cace.

12. Mudzibzalire m'cilungamo mukolole monga mwa cifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, nabvumbitsira inu cilungamo.

13. Mwalima coipa, mwakolola cosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakati watama njira yako ndi kucuruka kwa anthu ako amphamvu.

14. Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribeli; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ace.

15. Momwemo adzakucitirani Betele, cifukwa ca coipa canu cacikuru; mbanda kuca mfumu ya Israyeli idzalikhika konse.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 10