Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Habakuku 2:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndiponso vinyo ngwonyenga, ngati munthu wodzikuza, wosakhala kwao; wakukulitsa cikhumbo cace ngati kunsi kwa manda, akunga imfa, yosakhuta, koma adzisonkhanitsira amitundu onse, nadzimemezera mitundu yonse ya anthu.

6. Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wocurukitsa zimene siziri zace! mpaka liti? iye wodzisenzera zigwiriro.

7. Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao?

8. Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.

9. Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yace phindu loipa, kuti aike cisanja cace ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la coipa!

10. Wapangira nyumba yako camanyazi, pakuononga mitundu yambiri ya anthu, ndipo wacimwira moyo wako.

11. Pakuti mwala wa m'khoma upfuula, ndi mtanda wa kuphaso udzaubvomereza.

12. Tsoka tye wakumanga mudzindi mwazi, nakhazikitsa mudzi ndi cisalungamo!

13. Taonani, sicicokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto nchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pace?

14. Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi cidziwitso ca ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi panyanja.

15. Tsoka wakuninkha mnzace cakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!

Werengani mutu wathunthu Habakuku 2