Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Habakuku 2:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang'anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha ciani pa coneneza canga.

2. Ndipo Yehova anandiyankha nati, Lembera masomphenyawo, nuwacenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira.

3. Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pace, osanama; akacedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.

4. Taonani, moyo wace udzikuza, wosaongoka m'kati mwace; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa cikhulupiriro cace.

5. Ndiponso vinyo ngwonyenga, ngati munthu wodzikuza, wosakhala kwao; wakukulitsa cikhumbo cace ngati kunsi kwa manda, akunga imfa, yosakhuta, koma adzisonkhanitsira amitundu onse, nadzimemezera mitundu yonse ya anthu.

Werengani mutu wathunthu Habakuku 2