Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 9:14-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo padzakhala popimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo;

15. ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene liri ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse cigumula cakuononga zamoyo zonse.

16. Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lacikhalire liri ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi.

17. Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ici ndici cizindikiro ca pangano ndalikhazikitsa popaogana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.

18. Ndi ana amuna a Nowa amene anaturuka m'cingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wace wa Kanani.

19. Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.

20. Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa:

21. namwa vinyo wace, naledzera; ndipo anali wamarisece m'kati mwa bema wace.

22. Ndipo Hamu atate wace wa Kanani, anauona umarisece wa atate wace, nauza abale ace awiri amene anali kunja.

23. Semu ndi Yafeti ndipo anatenga copfunda, naciika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda cambuyo, napfunditsa umarisece wa atate wao: nkhope zao zinali cambuyo, osaona umarisece wa atate ao.

24. Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwace, nadziwa cimene anamcitira iye mwana wace wamng'ono.

25. Ndipo anati,Wotembereredwa ndi Kanani:Adzakhala kwa abale ace kapolo wa akapolo:

26. Ndipo anati:Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu;Kanani akhale kapolo wace.

27. Mulungu akuze Yafeti,Akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wace.

28. Ndipo Nowa anakhala ndi moyo cigumula citapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu.

29. Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.

Werengani mutu wathunthu Genesis 9