15. Mulungu ndipo ananena kwa Nowa, kuti,
16. Turukamoni m'cingalawamo, iwe ndi ana ako, ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.
17. Turutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse ziti ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi; kuti ziswane pa dziko lapansi, zibalane, zicuruke pa dziko lapansi.
18. Ndipo anaturuka Nowa ndi ana ace, ndi mkazi wace, ndi akazi a ana ace, pamodzi naye:
19. zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa pa dziko lapansi, monga mwa mitundu yao, zinaturuka m'cingalawamo.
20. Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.
21. Ndipo Yehova anamva conunkhira cakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwace, Sindidzatembereranso konse nthaka cifukwa ca munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata wace; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndacitiramo.
22. Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, cisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.