Ndipo Yehova anamva conunkhira cakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwace, Sindidzatembereranso konse nthaka cifukwa ca munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata wace; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndacitiramo.