1. Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'cingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi;
2. ndipo anatsekedwa akasupe a madzi akuru ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kwuwamba;
3. ndipo madzi anaphweraphwerabe pa dziko lapansi: pamene anatha masiku zana limodzi kudza makumi atatu madzi anacepa.
4. Ndipo cingalawa cinaima pa mapiri a Ararati, mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi.
5. Ndipo madzi analinkucepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.
6. Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la cingalawa limene analipanga:
7. ndipo anaturutsa khungubwe, ndipo anaturuka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi,
8. Ndipo anaturutsa njiwa imcokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi;
9. koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lace, nibwera kwa iye kucingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anaturutsa dzanja lace, naitenga, nailowetsa kwa iye m'cingalawamo.