Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 6:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Uike zenera m'ciogalawaco, ulimarize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pace: khomo la cingalawa uike m'mbali mwace; nucipange ndi nyumba yapansi, ndi yaciwiri, ndi yacitatu.

17. Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa cigumula ca madzi pa dziko lapansi, kuti cionooge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa.

18. Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'cingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.

19. Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiri ziwiri za mtundu wao ulowetse m'cingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 6