Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 46:3-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Aigupto; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukuru;

4. Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Aigupto; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lace pamaso pako.

5. Ndipo Yakobo anacoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israyeli anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magareta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye,

6. Ndipo anatenga ng'ombe zao ndi cuma cao anacipezam'dziko la Kanani, nadza ku Aigupto, Yakobo ndi mbeu zace zonse pamodzi ndi iye;

7. ana ace amuna, ndi zidzukulu zace zazimuna, ndi ana akazi ace, ndi zidzukulu zace zazikazi, ndi mbeu zace zonse anadza nazo m'Aigupto.

8. Maina a ana a Israyeli amene anadza m'Aigupto ndi awa: Yakobo ndi ana amuna ace: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.

9. Ndi ana amuna a Ruberu Hanoki, ndi Palu, ndi Hezroni, ndi Karmi.

10. Ndi ana amuna a Simeoni: Yemueli ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Sauli, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.

11. Ndi ana amuna a Levi: Gerisoni, Kohati, ndi Merai.

12. Ndi ana amuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana amuna a Perezi ndiwo Hezroni ndi Hamuli.

13. Ndi ana amuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Yabi, ndi Simroni.

14. Ndi ana amuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaledi.

15. Amenewo ndi ana amuna a Leya, amene anambalira Yakobo m'Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wace Dina; ana amuna ndi akazi onse: ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.

16. Ndi ana amuna a Gadi: Zifioni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Ezboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.

17. Ndi ana amuna a Aseri: Yimna, ndi Yisiva, ndi Yisivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Maliki eli.

Werengani mutu wathunthu Genesis 46