Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 45:7-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m'dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi cipulumutso cacikuru.

8. Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lace lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Aigupto.

9. Fulumirani, kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Cotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Aigupto lonse: tsikirani kwa ine, musacedwe.

10. Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;

11. ndipo ndidzacereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.

12. Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndirikulankhula ndi inu.

13. Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Aigupto, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.

14. Ndipo anagwa pakhosi pace pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pace.

15. Ndipo anampsompsona abale ace onse, nalilira iwo; ndipo pambuyo pace abale ace onse anaceza naye.

16. Ndipo mbiri yace inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ace a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ace.

17. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Citani ici; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani;

18. katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Aigupto, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.

19. Tsopano mwalamulidwa citani ici; muwatengere ana anu ndi akazi magareta a m'dziko la Aigupto; nimubwere naye atate wanu.

20. Musasamalire cuma canu; popeza zabwino za dziko lonse la Aigupto ndi zanu.

21. Ndipo ana a Israyeli anacita cotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magareta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira,

22. Onse anawapatsa yense zobvala zopindula; koma Benjamini anampatsa ndalama zasiliva mazana atatu ndi zobvala zopindula zisanu.

23. Kwa atate wace anatumiza zotere: aburu khumi osenza zinthu zabwino za m'Aigupto, ndi aburu akazi khumi osenza tirigu, ndi cakudya, ndi phoso la atate la panjira.

Werengani mutu wathunthu Genesis 45