Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 45:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo ana a Israyeli anacita cotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magareta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira,

22. Onse anawapatsa yense zobvala zopindula; koma Benjamini anampatsa ndalama zasiliva mazana atatu ndi zobvala zopindula zisanu.

23. Kwa atate wace anatumiza zotere: aburu khumi osenza zinthu zabwino za m'Aigupto, ndi aburu akazi khumi osenza tirigu, ndi cakudya, ndi phoso la atate la panjira.

24. Ndipo anamukitsa abale ace, ndipo anacoka; ndipo anati kwa iwo, Musakangane panjira.

25. Ndipo anakwera kuturuka m'Aigupto, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao.

26. Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Aigupto, Pamenepo mtima wace unakomoka, pakuti sanawakhulupirira iwo.

27. Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magareta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;

Werengani mutu wathunthu Genesis 45