Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 43:29-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo iye anatucula maso ace naona Benjamini mphwace, mwana wa amace, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akucitire we ufulu, mwana wanga.

30. Ndipo Yosefe anafulumira, cifukwa mtima wace unakhumbitsa mphwace, ndipo mafuna polirira; nalowa m'cipinda ace naliramo.

31. Ndipo anasamba ikhope yace, naturuka; ndipo anadziletsa, nati, Ikani cakudya.

32. Ndipo anamuikira iye cace pa yekha, ndi wo cao pa okha, ndi Aaigupto ikudya naye cao pa okha; cifukwa aigupto sanathei kudya cakudya pamodzi ndi Ahebri: cifukwa kucita comweco nkunyansira Aaigupto.

33. Ndipo anakhala pamaso pace, woyanba monga ukuru wace, ndi wanng'ono mensa ung'ono wace; ndipo mazizwa wina ndi wina.

34. Ndipo mawagawira mitanda ya patsogolo pace; koma mtanda wa Benjamini maposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 43