Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 43:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu cifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.

15. Amunawo ndipo anatenga mphatso, natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Aigupto, naima pamaso pa Yosefe.

16. Ndipo pamene anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wace, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakoozere, cifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.

17. Munthuyo anacita monga anamuuza Yosefe, ndipo munthuyo analowa nao anthuwo m'nyumba ya Yosefe.

18. Anthuwo ndipo anaopa, cifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Cifukwa ca ndalama zila zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone cifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi aburu athu.

19. Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,

20. Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula cakudya:

21. ndipo panali pamene ife tinafika padgono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lace, ndalama zathu mkulemera kwace; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.

22. Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule cakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu.

23. Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu, ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu cum a m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawaturutsira Simeoni.

24. Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa aburu ao cakudya.

Werengani mutu wathunthu Genesis 43