Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 42:26-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo anasenzetsa aburu ao tirigu wao nacokapo.

27. Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lace kuti adyetse buru wace pacigono, anapeza ndalama zace; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lace.

28. Ndipo iye anati kwa abale ace, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, ziri kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzace kuti, Nciani ici Mulungu waticitira ife?

29. Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;

30. kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankharwe, natiyesa ife ozonda dziko.

31. Koma ife tinati kwa iye, Tiru anthu oona; sitiri ozonda;

32. tiri abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani.

33. Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;

34. idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: comweco ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzacita malonda m'dziko muno.

35. Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lace; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa,

36. Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzacotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.

Werengani mutu wathunthu Genesis 42