Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 40:13-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe nchito yako; ndipo udzapereka cikho ca Farao m'dzanja lace, monga kale lomwe m'mene unali wopereka cikho cace.

14. Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipoundicitiretu ine kukoma mtima: nundichule ine kwa Farao, nunditurutse ine m'nyumbamu:

15. cifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinacite kanthu kakundiikira ine m'dzeniemu.

16. Pamene wophika mkate anaona kuti mmasuliro wace unali wabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malicero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga;

17. m'licelo lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundu mitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'licelo la pamutu panga.

18. Ndipo Yosefe anayankha nati, Mmasuliro wace ndi uwu: malicelo atatu ndiwo masiku atatu;

19. akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuucotsa, nadzakupacika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.

20. Ndipo panali tsiku lacitatu ndilo tsiku lakubadwa kwace kwa Farao, iye anakonzera anyamata ace madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka cikho wamkuru, ndi mutu wa wophika mkate wamkuru pakati pa anyamata ace.

21. Ndipo anabwezanso wopereka cikho ku nchito yace; ndipo iye anapereka cikho m'manja a Farao.

22. Koma anampacika wophika mkate wamkuru; monga Yosefe anawamasulira.

23. Koma wopereka cikho wamkuru sanakumbukira Yosefe, koma anamuiwala.

Werengani mutu wathunthu Genesis 40