Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 40:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. ndipo cikho ca Farao cinali m'dzanjalanga: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'cikho ca Farao ndi kupereka cikho m'dzanja la Farao.

12. Ndipo Yosefe anati kwa iye, Mmasuliro wace ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;

13. akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe nchito yako; ndipo udzapereka cikho ca Farao m'dzanja lace, monga kale lomwe m'mene unali wopereka cikho cace.

14. Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipoundicitiretu ine kukoma mtima: nundichule ine kwa Farao, nunditurutse ine m'nyumbamu:

15. cifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinacite kanthu kakundiikira ine m'dzeniemu.

16. Pamene wophika mkate anaona kuti mmasuliro wace unali wabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malicero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga;

17. m'licelo lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundu mitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'licelo la pamutu panga.

18. Ndipo Yosefe anayankha nati, Mmasuliro wace ndi uwu: malicelo atatu ndiwo masiku atatu;

19. akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuucotsa, nadzakupacika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.

Werengani mutu wathunthu Genesis 40