Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 4:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.

18. Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke.

19. Ndipo Lameke anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lace la wina ndi Ada, dzina lace la mnzace ndi Zila.

20. Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe,

21. Ndi dzina la mphwace ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oyimba zeze ndi citoliro.

22. Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a citsulo; mlongo wace wa Tubala-Kaini ndi Nama.

23. Lameke ndipo anati kwa akazi ace:Tamvani mau anga, Ada ndi Zila;Inu akazi a Lameke, mverani kunena kwanga:Ndapha munthu wakundilasa ine,Ndapha mnyamata wakundiphweteka ine,

24. Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri,Koma Lameke makumi asanu ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Genesis 4