Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 4:11-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, Imene inatsegula pakamwa pace kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako:

12. pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yace: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi.

13. Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukuru kosapiririka.

14. Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.

15. Ndipo Yehova anati kwa iye, Cifukwa cace ali yense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika icizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe ali yense akampeza.

16. Ndipo Kaini anaturuka pamaso pa Yehova, ndipo anakhalam'dziko la Nodi, kum'mawa kwace kwa Edene.

17. Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.

18. Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke.

19. Ndipo Lameke anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lace la wina ndi Ada, dzina lace la mnzace ndi Zila.

20. Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe,

21. Ndi dzina la mphwace ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oyimba zeze ndi citoliro.

22. Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a citsulo; mlongo wace wa Tubala-Kaini ndi Nama.

23. Lameke ndipo anati kwa akazi ace:Tamvani mau anga, Ada ndi Zila;Inu akazi a Lameke, mverani kunena kwanga:Ndapha munthu wakundilasa ine,Ndapha mnyamata wakundiphweteka ine,

24. Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri,Koma Lameke makumi asanu ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Genesis 4