Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 4:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wace Hava: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.

2. Ndipo anabalanso mphwace Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.

3. Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova.

4. Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zace ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yace:

5. koma sanayang'anira Kaini ndi nsembe yace. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yace.

6. Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?

7. Ukacita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kucita zabwino, ucimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwace, ndipo iwe udzamlamulira iye.

8. Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwace. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwace, namupha,

9. Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga?

10. Ndipo anati, Wacita ciani? Mau a mwazi wa mphwako andipfuulira Ine kunthaka.

Werengani mutu wathunthu Genesis 4