Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 39:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyace, Taonani, mbuyanga sadziwa cimene ciri ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zace zonse m'manja anga;

9. mulibe wina m'nyumba wamkuru ndine; ndipo sanandikaniza ine kanthu, koma iwe, cifukwa kuti uli mkazi wace: nanga ndikacita coipa cacikuru ici bwanji ndi kucimwira Mulungu?

10. Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvera mkazi kugona naye kapena kukhala naye.

11. Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire nchito yace; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo.

12. Ndipo mkazi anagwira iye copfunda cace, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya copfunda cace m'dzanja lace nathawa, naturukira kubwalo.

13. Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti anasiya copfunda cace m'dzanja lace, nathawira kubwalo,

14. anaitana amuna a m'nyumba yace, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Mhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinapfuula ndi mau akuru:

15. ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kupfuula, iye anasiya copfunda cace kwa me nathawira kubwalo.

16. Ndipo anasunga copfunda cace cikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyace.

17. Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, nati, Analowa kwa ine kapolo wa Cihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine:

Werengani mutu wathunthu Genesis 39