Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 39:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kupfuula, iye anasiya copfunda cace kwa me nathawira kubwalo.

16. Ndipo anasunga copfunda cace cikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyace.

17. Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, nati, Analowa kwa ine kapolo wa Cihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine:

18. ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kupfuula, iye anasiya cobvala cace kwa ine, nathawira kunja.

19. Ndipo panali pamene mbuyace anamva mau a mkazi wace, amene ananena kwa iye, kuti, Coteroci anandicitira ine kapolo wako; kuti iye anapsya mtima.

20. Ndipo mbuyace wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.

21. Koma Yehova anali ndi Yosefe namcitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang'anira kaidi.

22. Ndipo woyang'anira kaidi anapereka m'manja a Yosefe akaidi onse okhala m'kaidimo, ndipo zonse iwo anazicita m'menemo, iye ndiye wozicita.

23. Woyang'anira m'kaidi sanayang'anira kanthu kali konse kamene kanali m'manja a Yosefe, cifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazicita, Yehova anazipindulitsa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 39